SILVER YAKHUTIRA NDI POINT IMODZI
Timu ya Silver Strikers yati masewero awo ndi Mighty Wanderers tsopano ayamba kukhalano ovuta kamba koti chaka chatha ankangolepherana komabe akhutira ndi point imodzi koyenda.
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimuyi, Mapopa Msukwa, ndiye wanena izi kutsatira kuti alepherana 1-1 ndi Wanderers pa bwalo la Zomba.
Iye anati timu yake inasewera bwino mu chigawo chachiwiri koma akananika kugwiritsa ntchito mipata yomwe anapeza.
"Chigawo chachiwiri tinabwera osinthika ndipo tikanatha kugoletsa komabe kupeza point koyenda sizinaipe kwambiri ndipo takhutira," anatero Msukwa.
Kutsatira kupeza point imodziyi, Silver tsopano yafika pa mapoints khumi (10) mu ligi atapambana katatu, kufananitsa mphamvu kamodzi ndi kugonjanso kamodzi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores