SILWIMBA, NYONDO NDI CHOLOPI ADIKIRABE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wanderers, Bob Mpinganjira, wati ndi zokayikitsa kwambiri kuti osewera omwe achira, Clement Nyondo, Timothy Silwimba ndi Peter Cholopi apezeka pa masewero awo ndi Silver Strikers kamba koti akufuna kuwapatsa nthawi.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero omwe akumane ndi Mabanker ku bwalo la Zomba lamulungu masana ndipo wati osewerawa sapezeka pa masewerowa kuti azikokere minyewa yawo.
Komabe Mpinganjira wati akudziwa kuti Silver Strikers yakhala ikuchita bwino pamwamba pa timu yawo koma akayesetsa kuti achite bwino pa masewero alero.
"Tikudziwa kufunikira koti tichite bwino mmasewerowa chifukwa zitithandiza kwambiri mu ligimu nde chomwe titayesetse panopa ndikuti tichite bwino basi," anatero Mpinganjira.
Timuyi yasewerako masewero atatu mu ligi yaikulu ya mdziko muno ndipo yapambana kawiri ndi kugonja kamodzi ndipo azilowa mu masewerowa ali pa nambala 7 ndi mapoints asanu ndi imodzi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores