"NDIKUKHULUPIRA KUTI TIKACHITA BWINO" - MAKAWA
Mphunzitsi watimu ya Civil Service United, Abbas Makawa, wati akhulupilira kuti timu yake itakasewera ngati momwe anachitira mu chigawo chachiwiri ndi FCB Nyasa Big Bullets atha kukachita bwino ku Dedza.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Goshen City Dedza Dynamos lamulungu pa bwalo la Dedza ndipo wati akuyembekeza kuti akakhala masewero ovuta.
Iye wati kupambana komwe anakupeza ligi isanayambe siwapangitsa kuti ayiderere Dedza koma apita ndi mtima wofuna kukachita bwino.
"Ndi Bullets mu chigawo choyamba tinali achiwiri pa mpira komanso tinaphonya kwambiri koma mchigawo chachiwiri tinali bwino mwinanso ndi chifukwa tibamwetsa zigoli ziwiri nde ngati tikasewere momwemo tikachita bwino," iye anatero.
Matimuwa anakumana mu mpikisano wa chigawo chapakati pa bwalo lomweli ndipo Civil inapambana 3-0 kuti akhale akatswiri.
Timuyi ili pa nambala 6 ndi pointi imodzi imene anayipeza atalepherana ndi Bullets 2-2.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores