"TIMU YATHU NDI YOKONZEKA" - MAKAWA
Mphunzitsi watimu ya Civil Service United, Abbas Makawa, wati timu yake ndi imene ikufunitsitsa kwambiri chipambano kusiyana ndi FCB Nyasa Big Bullets kamba koti iwo akusewera pakhomo.
Iye amayankhula patsogolo pa kuyamba ligi ya FDH Premiership loweruka pa bwalo la Civo pokumana ndi Bullets ndipo wati akukhulupilira kuti ndi wokonzeka pa masewerowa.
Makawa watinso angakhale kuti timu yawo yataya osewera angapo omwe anali odalilika kutimuyi, akwanitsa kupeza osewera omwe awathandizire bwino mu chakachi.
"Tinataya osewera pafupifupi asanu ndi atatu odalilika ndipo palinso ena omwe sitikuwawerengeranso kwambiri koma omwe tapeza tawayesa akuoneka kuti tivutika koma pang'ono podikira kuti agwirane," Iye anatero.
Iye wamemanso ochemerera a timuyi kukhamukira pa bwalo la Civo kudzawachemerera pa masewerowa.
Timuyi inathera pa nambala yachisanu chaka chatha ndipo ikufunitsitsa kuyamba mwapamwamba mu chaka chino.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores