Haiya akulingalira zotengera omuyipitsira mbiri ku khothi
Mtsogoleri wa bungwe la Football Association of Malawi, Fleetwood Haiya, wati akufufuza kwa akatswiri ake pa zamalamulo kuti atengere anthu ena omwe akufuna azimuyipitsira mbiri ku bwalo la milandu.
Iye amayankhula izi lachitatu ku Chiwembe pomwe wati ndi okhumudwa kuti anthu ena odziwa kale komanso oyendetsa mpiranso akumayankhula zofuna kumuyipitsira mbiri yake.
Iye wati anthu ake ndi oti amayankhulana nawo ndipo ena amawathandiza kwambiri koma akangopanga kukwanilitsa zomwe amafuna, amamutembenukira ndi nkhani zabodza.
Iye wafotokozanso kuti Scorchers ili mmanja mwa FAM ndipo bungwe la National Womens Football Association ndi loyang'anira ma ligi a mpira wa amayi.
"Ndi chimodzimodzi kumanena kuti Flames yapita ku AFCON bwanji simunawabereke a Mitawa. Ineyo sindigwetseka kaya mukuti mwalowa m'boma, boma ndi la aliyense," anatero Haiya.
Iye anatinso anthu akupanga nkhani za iwo kuti akuwasala a Adellaide Migogo koma zili
[DELETED]
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores