"AKHALA MASEWERO OOPSA KOMA SITIKUWAOPA" - MGANGIRA
Mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter Mgangira, wati anyamata ake ndi okonzeka kukumana ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets pomwe wati akudziwa kuti akukumana ndi timu yabwino komabe sakuwaopa.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero a matimuwa masana a lamulungu pa bwalo la Kamuzu ndipo wati achita chilichonse chothekera kuti apeze ma pointsi onse atatu pa masewerowa.
"Chimene tikuyang'ana ife ndi choti tichepetse mpata wathu ndi kumtundako mukudziwa tikuteteza chikhochi nde masewero ake ndi amenewa omwe amapangitsa timu kuti itenge chikho nde tiyesetsa ndithu," anatero Mgangira.
Iye wati anyamata ake onse alibwino mu timuyi ndipo akungoyang'ana kuti ndi ati omwe akhale akutumikira mmasewerowa kuti awapatse zotsatira zabwino.
Timuyi ikupita mmasewerowa ili pa nambala yachitatu mu ligi ndi mapointsi okwana 36 pa masewero 17 omwe yasewera ndipo ikuchepekedwa ndi mapointsi asanu ndi awiri pa Bullets yomwe ili pamwamba.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores