Bwalo la Mzuzu ndi Mpira atsegulidwanso
Ma bwalo a Mzuzu komanso Mpira akuyembekezeka kuyamba kuchititsanso masewero akulu-akulu m'dziko muno pomwe bungwe la Football Association of Malawi lavomera kuti ma bwalowa tsopano ali pa mulingo wabwino.
Malingana ndi uthenga kuchokera ku bungweli, Komiti yoyang'anira za zoyenereza zoyenera ku matimu yavomera ma bwalowa kutsatira mkumano wawo wa lachiwiri lapitali pomwe anayendera ma bwalowa.
Bwalo la Mzuzu linatsekedwa mu mwezi wa July kutsatira kuonongeka kwa bwaloli pomwe kunali kukumbukira tsiku lokonderera ufulu wa dziko lino ndipo galimoto zinapondaponda pa bwalo losewerera.
Ndipo bwalo la Mpira ku Chiwembe linakanika kudutsa mulingo woyenerera poti ku zimbudzi za bwaloli kunabedwa chilichonse ndipo bungweli limagulako.
Matimu a Moyale Barracks komanso Mzuzu City Hammers omwe amagwiritsa bwalo la Mzuzu amakakamizika kupita ku Rumphi pa masewero awo a pakhomo pomwe Mighty Tigers, Ekhaya FC, Mighty Wanderers ndi FCB Nyasa Big Bullets o
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores