Silver ikunyamuka lero
Timu ya Silver Strikers ikunyamuka masana a lero kulowera m'dziko la Mauritius komwe akukasewera ndi timu ya Elgeco Plus mu chikho cha CAF Champions League lamulungu likudzali.
Timuyi yalengeza za nkhaniyi kudzera pa tsamba lawo la mchezo pomwe yatsimikiza kuti akafika lachinayi mu dzikoli.
Awa ndi masewero oyamba mu ndime yoyamba yachipulula ndipo masewero achibwerenza adzakhalako m'dziko muno sabata yotsatirayo.
Timuyi inyamuka nthawi ikamati 14:20hrs.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores