"NDINE WOKONDWA NDI MMENE ANYAMATA AKUSEWERERA" - CHINGOKA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Victor Chingoka, wati ndi wokondwa ndi mmene timu yake ikusewerera koma wafunira zabwino timu ya Mighty Mukuru Wanderers pomwe ikupitilira mu Chikho cha Castel.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe anagonja 3-0 ndi Manoma pa bwalo la Kamuzu ndipo wati kumbuyo kwa timuyi ndi kumene kunavuta mmasewerowa.
"Anali masewero abwino kwambiri, tinasewera bwino kwambiri ndipo ndine okondwa ndi mmene anyamata akusewerera pano koma mwina mphindi zisanu zakumapeto mchigawo choyamba kumbuyo kwathu kunagona koma zimachitika mu mpira tingoifunira zabwino Wanderers." Anatero Chingoka.
Timuyi tsopano yamaliza masewero ake a chaka cha 2023 ndipo akuyembekeza kukapumira kukonzekera ligi ya chaka cha 2024 pomwe anapulumuka pa tsiku lotsiliza lenileni mu ligi.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores