MOYALE YAKONDWA NDI KUTSEGULIDWA KWA BWALO LA MZUZU
Timu ya Moyale Barracks yati ili ndi chimwemwe kamba ka kuvomerezedwa kwa bwalo la Mzuzu poti zithandizira kuti timuyi ichite bwino kwambiri.
Wachiwiri kwa mlembi wamkulu kutimuyi a Kelvin Chisaka wati timuyi imaononga zinthu zochuluka kwambiri kukasewera ku Rumphi komwe amasewera ngati bwalo lawo mu masewero apakhomo.
Iye wati kubwereranso ziwathandizira kuchepetsa ndalama zomwe anaononga kuti asewere mmasewero awo.
"Ku Rumphi timayang'ana za mayendedwe komanso ogona koma pano tichepetsa zambiri zomwe tsopano zipite kosamalira umoyo wa osewera," anatero Chisaka.
Iye watinso masapota ndi anthu okonda masewero ku Mzuzu akhalanso okondwa kamba koti samakwanitsa kukaonera nawo masewero amatimu amu mzinda wa Mzuzu.
Kupatula timu ya Moyale, matimu a Mzuzu City Hammers komanso Embangweni United omwe amasewera mu NBS Bank National Division league nawo akhala akugwiritsa ntchito bwaloli ngati pakhomo mu ligi yawo.
Bungwe la Football As
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores