Blue Eagles ikuyembekeza Bullets yokwiya
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, De Kleck Msakakuona, wati akudziwa kuti timu ya FCB Nyasa Big Bullets ibwera movuta kwambiri mu masewero akukumana kamba koti inatengeredwa mapoints anayi Chaka chatha koma ndi okonzeka mmasewerowa.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo omwe aseweredwe pa bwalo la Civo loweruka masana.
Msakakuona wati timu yake ikudziwa kufunikira koti achite bwino pa masewerowa ndipo ayesetsa kuti anagonjetse Bullets.
"Ndine wokhutira ndi momwe timu ikuchitira komabe tikuyenera kumagoletsano zigoli zambiri chifukwa tikugoletsa zochepa," anatero Msakakuona.
Iye wati masewero omwe timuyi inali nawo mmaboma a Chikwawa ndi Nsanje awapatsanso kukonzeka kwabwino ndipo akuyembekeza kuchita bwino.
Eagles ili pa nambala yachiwiri ndi mapoints 9 pa masewero anayi mu Ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores