Timu ya Blue Eagles inalepherana ndi timu ya Nchalo Select lachitatu pa chikonzero chawo chobweretsa bata ku maboma a Chikwawa ndi Nsanje powadziwitsa kuti maliseche samasowa.
Timuyi inakonza masewerowa pofuna kukometsera uthenga womwe anatengawu ndipo osewera onse odalilika atimuyi anasewera nawo mmasewerowa.
Davie Tobias anatsogoza Nchalo Select kudzera pa penate pa mphindi 24 koma Webster Nzunda anabwenza kutangotha mphindi zitatu.
Uthengawu ukubwera kutsatira mchitidwe womwe anthu ammabomawa amachita pomwe amapha anthu omwe amati akuwaganizira kuti akumaba ziwalo za anthu koma zili zabodza.
Timuyi ikuyembekezeka kubwerera ku Lilongwe komwe ikukalandira FCB Nyasa Big Bullets pa bwalo la Civo kumathero a sabatayi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores