"TAGONJA KOMA SIKUTI TATAYIKA" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Prichard Mwansa, wati kugonja kwawo ndi Silver Strikers sikuti atayika koma tsopano ndi ntchito ya aphunzitsi Kuti akonze zinthu pa masewero 28 omwe atsala mu ligi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 4-1 pa bwalo la Silver ndipo wati zinangowavuta kuti mchigawo chachiwiri kunali kutayilira koma sikuti anasewera moyipa.
"Mchigawo choyamba tasewera mwapamwamba ndipo taphonya mipata koma mchigawo chachiwiri kunali kulekerera mwina osewera achisodzerawa anakanika kuti adekhe koma kuno ndi koyambilira tikonza," anatero Mwansa.
Iye wati tsopano azipatsa ntchito yoti osewerawa abwererenso mchimake ndikuti akamadzakumana ndi Chitipa United sabata ya mawa adzachite bwino.
Moyale ili pa nambala 13 mu ligi ndi point imodzi pa masewero awiri omwe yasewera mu ligi ya Chaka chino.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores