"MZIMU WOSEWERA UNACHOKAMO" - MHONE
Mphunzitsi watimu ya Kamuzu Barracks, Tione Mhone, wati timu yake inabalalika ndi kuchedwa kuyamba kwa masewero awo pomwe anauzidwa kuti masewero alephereka kenako ndi kuyambiranso.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-0 ndi Silver Strikers pa bwalo la Champions pa masewero omwe anakhala mphindi 53 asanayambe kudutsa nthawi yake yoyenerereka.
Pa masewerowa, timu ya Silver Strikers inapezeka kuti yaiwala makadi awo zomwe zinachititsa kuti masewero achedwe kuyamba ndipo Mhone wati zinawakhudza kwambiri osewera ake.
"Lero tivomereze sitinali bwino chifukwa cha chiyambi chifukwa takaongola minyewa ndikubwereranso kukakhala pafupifupi ola limodzi nde zonsezo zinawachotsa osewera mtima wosewera," anatero Mhone.
Komabe iye wati waona mavuto omwe timu yake yakumana nawo pa masewerowa ndipo ayesetsa kukonza kuti kutsogoloku achite bwino.
KB ili pa nambala 16 mu ligi opanda point iliyonse ndipo akumana ndi Mitundu Baptist mu masewero awo achiwir
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores