Kudonto waonjezera mgwirizano wake
Katswiri wosewera pakati ku timu ya Mighty Wanderers, Dan Kudonto, waonjezera mgwirizano wake ndi zaka ziwiri kutimuyi lolemba masana.
Kudonto anali ndi mgwirizano wozatha chaka cha 2026 kusemphana ndi zomwe masamba ena amalemba ndipo waonjezera kuti akhalabe kutimuyi kufikira mu 2028.
Iye anachokera kutimu yaing'ono ya Wanderers ndipo wakhala wofunikira mu chaka cha 2025 pomwe wayithandizira timuyi kutenga ukatswiri wa Supa ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores