Kaliati afika mpaka zaka 12 ali ku Manoma
Katswiri wosewera pakati kutimu ya Mighty Wanderers, Isaac Kaliati waonjezera mgwirizano wake ndi timuyi pomwe akhalabe kufikira mu chaka cha 2027.
Timuyi yalengeza za nkhaniyi lolemba madzulo pomwe Kaliati akhalebe mpaka zaka 12 ndi timuyi poti anapitako mu 2015 kuchokera ku Mighty Tigers.
Katswiriyu anakana mwayi wopita kunja kwa dziko lino pomwe Simba Bhora imamufuna koma wasankhabe kukhala kutimuyi.
Iye wathandizira timuyi kupambana zikho zosiyanasiyana kuphatikizirako ligi kawiri mu 2017 ndi chaka chino.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores