Chitipa United yavuta pa Lewa Nkosi
Wosewera yemwe timu ya Ekhaya FC amusaina kumene, Lewa Nkosi, akhonza kuchedwa kuti atumikire timuyi kamba koti timu ya Chitipa United yavuta potengera kuti ndi osewera wawo.
Malipoti akuonetsa kuti osewerayu anapita pa ngongole kutimu ya Songwe Border United koma wakhala wa Chitipa kuchokera mu 2023 pomwe anasaina mgwirizano wake.
Ndipo timuyi sinakhutire ndi malonda pakati pa Ekhaya ndi Songwe zomwe zachititsa kuti asapatsidwe mapepala ake omuloleza kusewera ku Ekhaya mpaka zonse ziyende bwino.
Nkosi anadziwika kwambiri pomwe timu ya Songwe inagonja 7-0 ndi FCB Nyasa Big Bullets Koma anasewera mwapamwamba mpaka kupatsidwa ndalama ndi ochemelera a Bullets.
Source: Sports Battalion
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores