NTOPWA YAKHALA AKATSWIRI KUMMWERA
Timu yomwe imasewera mpira wamiyendo koma ali amayi, Kukoma Ntopwa Super Queens, yakhala akatswiri a chikho cha FAM Women's Championship yakummwera kwa dziko lino kutsatira kugonjetsa Red Lioness 6-0 pa bwalo la Kamuzu lamulungu.
Timuyi imangofunikira kupambana basi kuti azisiyana mapointsi asanu ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets Women ndipo imachita m'batizo waukulu kwa atsikana aku Zombawa.
Ntopwa yapambana masewero awo onse 13 ndipo yakwanitsa kupeza mapointsi okwana 39 ndipo mmasewero awo omaliza akumana ndi Bullets Women yomwe ili pa nambala yachiwiri ndi mapointsi 34 mu chikhochi.
Zateremu, Ntopwa yafika pa ndime ya dziko lonse ya mpikisanowu ndipo matimu awiri ena omwe ali pachiwiri ndi pachitatu ngati FCB Nyasa Big Bullets Women komanso Mighty Wanderers Ladies afikanso pa ndimeyi.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores