OSEWERA A BULLETS ALANDIRA K0.2 MILLION ALIYENSE AKAPHA TP MAZEMBE
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yalonjeza osewera awo kuti apatsidwa ndalama yoonjezera yokwana MK200,000 aliyense ngati agonjetse timu ya TP Mazembe masana a lamulungu pa bwalo la Bingu ku Lilongwe.
Mkulu oyendetsa ntchito za timuyi, Albert Chigoga, wati osewera atimuyi akonzekera kwambiri kwambiri ndipo ndi zomwe apatsidwa, akonzeka kugwetsa Mazembe mu CAF Champions league. Iye wathokozanso osewera akale, Kinnah Phiri ndi Lawrence Waya kamba kodzawalimbikitsa osewerawa.
"Tili ndi chikhulupiliro kuti osewerawa agwira ntchito chifukwa chilichonse apatsidwa. [Kinnah ndi Lule] sitinawaitane koma anangoona okha kuti abwere adzawalimbikitse osewera athu, tikuwathokoza kwambiri." Anatero Chigoga.
TP Mazembe inafika mdziko muno lachinayi patsogolo pa ndime yoyamba ya masewero a CAF Champions league ndipo otsatira azachitika ku DRC konko.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores