BULLETS YAKANA PAMWAMBA
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yagonja koyamba mu ligi ya FDH Premiership pomwe yagonja 1-0 ndi timu ya Goshen City Dedza Dynamos pa bwalo la Dedza loweruka masana.
Chigoli cha Marcos Chiwaya cha pa mphindi 41 mu chigawo choyamba chinali chokwana kukaniza Bullets chipambano zomwe zawapangitsa kukanika kufika pamwamba pa ligi.
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimuyi Heston Munthali anavomera kuti timu yake sinasewere bwino zomwe ndi zokhumudwitsa kwambiri.
"Kukamba za kaseweredwe sikanali bwino chifukwa zimakhala ngati anyamata tikuchita kuwakakamiza, amalemedwa komanso ziganizo zinali zolakwika zomwe zimachititsa kuti tisamenyere pagolo," anatero Munthali.
Iye anatinso sizinayende bwino chifukwa samayenera kugonja masewerowa ndipo awayankhula osewera awo za nkhaniyi ndi kuwauza kuti azitha kuikapo mtima kochuluka kuti azichita bwino kwambiri.
Zateremu, timuyi yatsika pomwe ili pa nambala yachinayi mu ndandanda wa matimu mu ligi pomwe ilibe ndi mapoints 20 pa zipa
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores