"OCHEMERERA ATHU TIWAPEPESA NDI CHIPAMBANO" - NYEMERA
Mphunzitsi wogwirizira watimu ya Goshen City Dedza Dynamos Lazarus Deco Nyemera wamema otsatira a timuyi kukafika ku bwalo la Dedza loweruka kuti akawapepese ndi chipambano kutsatira kuti anagonja sabata yatha.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero a timuyi ndi FCB Nyasa Big Bullets mu sabata 11 ya FDH Premiership.
Nyemera wati akudziwa kuti akhala masewero ovuta kwambiri koma ayesetsa kukonza mavuto omwe anawaona kuti achite bwino mu masewerowa.
"Kupambana ndekuti tifika pa mapoints 11 zomwe zikhale bwino ndiye masewero atha sitinawayambe bwino komabe tagwiragwira zonse zoyenereza kuchititsa kuti tikapambane," anatero Nyemera.
Iye wati akudziwa kuti masapota awo anakhumudwa atagonja ndi Chitipa United komabe timu ikadali bwino ndipo akapeza chipambano.
Dynamos ikulowa mmasewerowa ili pa nambala 14 ndi mapoints asanu ndi atatu mu masewero khumi omwe asewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores