MUNTHALI WALIMBITSA MTIMA MASAPOTA A BULLETS
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets Heston Munthali wati kukanika kupeza zipambano mu masewero ndi mbali imodzi ya mpira komabe ayesetsa kuti akakonze kuti zotsatira ziyambe kubweranso.
Iye amayankhula atatha masewero omwe alepherana 0-0 ndi timu ya Ekhaya ndipo ochemerera awo anaonetsa kusakhutira ndi kaseweredwe katimuyi mpaka kuyamba kugenda.
Iye wati timu yake ili ndi vuto la kugoletsa lomwe akhala akulikonza komabe satopa kuti zinthu ziyende bwino.
"Ku zokonzekera zathu zimaoneka bwino koma kubwera pa bwalo zosemphana nde uwu ndi mpira ndi mmene umakhalira tikungoyenera kuvomereza zotsatirazi palibe chomwe tingachite," anatero Munthali.
Iye anatinso mchigawo choyamba anavutika kwambiri ndi kaseweredwe koma mchigawo chachiwiri anachitabe bwino angakhale kuti sanagoletse.
Timuyi inali ndi mwayi wofika pamwamba pa ligi koma ili pachitatu ndi mapoints 20 pa masewero khumi omwe asewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores