KB YAIMITSA APHUNZITSI AKE
Timu ya Kamuzu Barracks yalengeza kuti yaimitsa kaye ntchito mphunzitsi wamkulu, Tione Mhone komanso wachiwiri wake Joseph Chilapondwa kamba ka kusachita bwino kwa timuyi.
Mu kalata yomwe yalembedwa lachiwiri madzulo ndipo yasainidwa ndi mlembi wamkulu Leutenant Blessings Sibanda yati kuimitsidwaku ndi kwa pompopompo.
Timuyi tsopano ikhala mwa Kenwood Nkhoma ngati wogwilizira kufikira pomwe timuyi ipange chiganizo chotsiliza.
Kamuzu Barracks yayamba moipa kwambiri mu ligi ya chaka chino pomwe yagonja ndi Silver Strikers 2-0 komanso LUANAR Mitundu 1-0 ndipo yafanana mphamvu 1-1 ndi Karonga United kuti akhale pa nambala 15 mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores