KB YALANGA OCHEMERERA, ASILIKALI AWO
Timu ya Kamuzu Barracks yapereka zilango kwa ochemerera komanso asilikali omwe anakhudzidwa pa kumenyedwa kwa opereka chitetezo pa masewero omwe anagonja 1-0 ndi LUANAR Mitundu lamulungu.
Mukalata yomwe wasaina ndi mlembi wamkulu wa timuyi, Lieutenant B. Sibanda, yati timuyi imakhulupilira kusunga mwambo, khalidwe komanso chitetezo cha anthu mbali zonse.
Iwo atsutsa mchitidwewu omwe unachitika pokhumudwa ndi penate yomwe oyimbira anapereka ku Mitundu ndipi ochemererawa anafuna kumugwiragwira oyimbira koma achitetezowa anawateteza.
KB yapereka chilango kwa ochemerera okhudzidwa chosapanga nawo masewero aliwonse okhudza Kamuzu Barracks kwa chaka chimodzi komanso chilango kwa asilikali okhudzidwa poti ndi zotsutsana ndi dongosolo logwilira ntchito la Malawi Defence Force.
Komabe mu kalatayi simunatchule mayina a anthuwa omwe apatsidwa chilango ndi timuyi.
Iwo apepesa kwa opereka chitetezo, LUANAR Mitundu FC, oyimbira, anthu aku Dedza ndi okonda m
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores