"TAVOMEREZA KUTI LERO SITINASEWERE BWINO" - MSAKAKUONA
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, De Kleck Msakakuona, wati timu yake sinasewere bwino pa masewero awo ndi timu ya Chitipa United ndi chifukwa chake agonja ndipo avomereza.
Iye amayankhula atatha masewerowa omwe anali pa bwalo la Chitipa ndipo agonja 1-0 ndi chigoli cha Joseph Mbaga loweruka masana.
Iye wati timu yake inakanika kugwilitsa ntchito mipata yomwe anayipeza mchigawo choyamba ndipo mchigawo chachiwiri sanali bwino.
"Apa tibwerera kuti tikakonze mavuto athu kuti tisawabwerenzenso mu masewero akudzawa koma tivomereze kuti lero sitinali bwino," anatero Msakakuona.
Timuyi tsopano yatsika kufika pa nambala yachinayi mu ligi yaikulu ya m'dziko muno pomwe ili ndi mapoints atatu atapambana kamodzi ndi kugonjanso kamodzi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores