KAMUZU BARRACKS YADANDAULA NDI OYIMBIRA
Timu ya Kamuzu Barracks yadandaula ndi ziganizo za oyimbira pa masewero omwe amasewera ndi timu ya LUANAR Mitundu kutsatira penate yomwe inaperekedwa kumapeto a masewerowa.
Pakutha pa masewero omwe agonja 1-0 kudzera pa penateyi, osewera ndi akuluakulu ena anakazungulira oyimbira kusakhutira ndi ntchito yawo koma achitetezo anakwanitsa kuwachotsapo ndipo akuluakulu ena a Kamuzu Barracks anakwanitsa kudekhetsa osewerawa.
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimuyi, Josephy Chilapondwa, wati ndalama ziononga masewero mu ligiyi pomwe oyimbira alawilira kupanga ziganizo zosayenera.
"Anali masewero abwino ndipo matimu onse amasewera bwino koma basi oyimbirawa kupanga ziganizo zawo apereka penate yabodza nde ndi zovuta kuzimvetsa," anatero Chilapondwa.
Awa anali masewero achiwiri timuyi kugonja pomwe sabata yatha anagonja 2-0 pa masewero omwenso anauzidwa kuti alephereka kamba koti Silver inayiwala makadi koma patadutsa mphindi 53, masewero anayamba.
Timuy
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores