Fazili akuyang'ana zokatenga COSAFA
Mphunzitsi watimu ya Scorchers, Lovemore Fazili, wati akuyang'ana zofika ndime yotsiriza kapena kutenga chikho kumene pomwe timuyi isewere mu mpikisano wa COSAFA mwezi wa mawa.
Iye amayankhula pomwe amayitana mayina a osewera 32 omwe ayambe m'bindikiro pa 4 February kukonzekera mpikisanowu.
Iye wati akuona kuthekera kochita bwino kwambiri chifukwa watenga osewera omwe ndi odziwa komanso akuchita bwino mu ligiyi.
"Sikuti tikungopita kokayenda ayi koma tikufuna tikafike mu ndime yotsiriza komanso kukatenga chikhocho. Tatenga osewera omwe akuchita bwino mu ligi yathu ya National Bank nde tikayesetsa ndithu," iye anatero.
Fazili watenga osewera a mdziko mommumo 28 komanso omwe amasewera kunja anayi ndipo adzasankha osewera omwe adzapite nawo pa ulendowu.
Mpikisanowu ukuyembekezeka kuyamba pa 18 February mdziko la South Africa ndipo Malawi yapambanako kamodzi chiyambireni mpikisanowu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores