CHAWINGA APHONYANA NDI ARSENAL
Katswiri wa timu ya Scorchers, Tabitha Chawinga, sapezeka pa masewero omwe OL Lyoness ikumane ndi timu ya Arsenal Women podzigulira malo mu ndime yotsiriza ya chikho cha UEFA Women's Champions League loweruka.
Chawinga sali mu gulu la osewera omwe agwire ntchito mu masewerowa kamba kovulala malingana ndi ndandanda womwe timuyi yatulutsa.
Katswiriyu anali panja pa masewero oyamba omwe matimuwa anakumana Ku dziko la England lamulungu lapitalo ndipo sanalowetsedwe mu masewero onse.
Timu ya Lyon ikulowa mmasewerowa ikugonja 2-1 ndipo ikuyang'ana zobwenza chipongwe kamba koti inatulutsidwanso mu ndime ya matimu anayi ndi Arsenal yomweyi chaka chatha.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores