"TIYESETSA KUTI TIPAMBANE PAKHOMO" - MGANGIRA
Mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter Mgangira, wati timu yake ikukumana ndi timu yovuta kwambiri komabe ayesetsa kuti achite bwino pogwiritsa ntchito mwayi wosewerera pakhomo.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero omwe akukumana ndi Moyale Barracks pa bwalo la Silver loweruka.
Iye wati timu yake yakonzekera bwino masewerowa ndipo akudziwa momwe akachitire poti akakumana ndi matimu achisilikali samafuna kuti timu yake izisunga mpira kwambiri.
"Tikukumana ndi timu yovuta yomwe ndi amkhala kale mu ligi komanso ili ndi aphunzitsi odziwa ntchito komabe kwa ife takonzekera kuti mwina tidzaonetse mwayi wosewerera pakhomo," anatero Mgangira.
Iye watinso ochemerera a timuyi akhamukire ku bwaloli kudzasapotera timuyi ndipo adzayesetsa kuti adzawapatse chimwemwe pakutha pa masewerowa.
Silver ili pamwamba pa ligi ndi mapointsi atatu kamba koti inapambana 2-0 ndi Kamuzu Barracks mu masewero oyamba.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores