Timu ya Kamuzu Barracks yalowa mu mgwirizano ndi banki ya NBS yomwe ikhale ikuthandiza timuyi mu ligi ya chaka chino ya FDH Premiership.
Izi zadziwika pa mwambo womwe timuyi pamodzi ndi kampaniyi unachititsa masana a lachisanu mu mzinda wa Lilongwe.
Mu mgwirizanowu, timuyi ikhale ikulandira ndalama zokwana K45 million ndipo dzina la bankiyi likhale likuoneka pa zovala za timuyi.
Bankiyi ikadapitilira kukhazikika Ku mpira wa mdziko muno pomwe amathandizanso ligi ya National Division League komanso Charity Shield.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores