KHUNGWA ALIPO, SAMA KULIBE POKUMANA NDI KARONGA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Mighty Wanderers, Macdonald Mtetemera, watsimikiza kuti wosewera wotchinga pagolo Dalitso Khungwa wachira ndipo Sama Thierry Tanjong sapezeka pa masewero awo ndi Karonga United.
Iye amayankhula lachisanu patsogolo pa masewero otsegulira ligiwa pa bwalo la Kamuzu mu mzinda wa Blantyre ndipo wati osewera ena monga Clement Nyondo, Timothy Silwimba ndi Chimwemwe Nkhoma akadakonzabe za kubwerera pa bwalo koma sapezeka.
Iye anatinso Khungwa alipo ndipo chiganizo ndi chawo kuti amukhazike pagolo kapena ayi koma wati timu yake yakonzeka bwino.
"Masewero athu ndi Bullets anatithandiza kuona momwe tinafooka ndipo takonza, titati tagwiritsa ntchito ndekuti tikapambana mosavuta mmasewerowa," Iye anatero.
Iye wati chomwe akuyang'ana ndi chipambano chokha ndi cholinga choti ayambe bwino mu ligi ya chaka chino.
Manoma ndi omwe akuteteza ukatswiri wa ligi pomwe anakwanitsa kupambana chaka chatha kumalizitsa nthawi
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores