PAIPI WATSANZIKA KU SILVER
Katswiri wotseka kumbuyo kutimu ya Silver Strikers, Maxwell Paipi, watsanzika kutimuyi pomwe tsopano akuyembekezeka kulowera mdziko la Zimbabwe kusiyana ndi timuyi.
Paipi akuchoka ku Silver mgwirizano wake utatha ndipo wakana kutikitira mgwirizano wina watsopano kuti akayese mwayi mu dziko la kunja.
Iye akuyembekezeka kupita ku timu ya FC Platinum yomwe anakambirana kale zonse mu miyezi yapitayo.
Iye akupita ku timu yomwe kumasewera Nickson Nyasulu ndi Precious Phiri ndipo yasiyana posachedwapa ndi Vincent Nyangulu.
Source: Twaha Silva Chimuka
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores