''TIDZASANGALALA TIKADZAPULUMUKA TSIKU LOTSILIZA'' - KAJAWA
Mphunzitsi watimu ya Mighty Tigers, Trevor Kajawa, wati ntchito ikadalipo yoti agwire ngakhale kuti atuluka mu chigwa cha matimu otuluka mu ligi ndipo adzasangalala zonse zikadzatha.
Iye amayankhula izi kutsatira kugonjetsa Kamuzu Barracks 1-0 lachitatu pa bwalo la Mpira lachitatu masana pomwe wati anakonzadi kuti apambane poti sali pabwino pa ndandanda wa matimu mu ligi.
Kajawa wati akuyenerabe kuikapo mtima poti mpikisano tsopano wakula zomwe zithabe kuwavuta ngati sasamala.
''Sitinapulumuke ayi ndipo ntchito ikadalipo ndekuti ifeyo sitingasangalale ayi, tikuyenera kuzidalira patokha osati kudaliranso timu ina ayi nde tidzasangalala ligi ikadzatha,'' anatero Kajawa.
Timuyi yasuntha kuchoka pa nambala 14 kufika pa 12 pomwe ili ndi ma pointsi okwana 26 atapambana kasanu ndi kamodzi, kufanana mphamvu kasanu ndi katatu ndi kugonja ka khumi ndi kamodzi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores