"Petro ndi osewera yemwe atithandize kwambiri" - Mgangira
Mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter Mgangira, wati osewera yemwe amusaina kumene Ernest Petro wachita bwino kwambiri pa zokonzekera pomwe achite kusankha ngati asewere kapena ayi koma ayithandiza kwambiri timuyi.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewero atimuyi ndi Chitipa United omwe aliko lachitatu mu ligi ndipo wati sikuti anangosaina kuti akutola koma amatenga osewera wapamwamba.
"Petro ndi osewera wabwino ndipo momwe timamusaina timadziwa kuthekera kwake, ndi osewera yemwe atithandize kwambiri osati kuti timangosainapo basi." Anatero Mgangira.
Iye wati akudziwa kuti akusewera ndi timu yomwe ili yabwino yomwe ukaphethira imatha kupambana koma ayesetsa kuti akagwiritse mipata yomwe akapeze kuti akapambane pakhomo.
Timuyi ili pa nambala yachitatu mu ligi pomwe ili ndi ma points okwana 33 pa masewero 16 omwe yasewera poti inapambana kasanu ndi kanayi (9), kufanana mphamvu kasanu ndi kamodzi ndi kugonja kamodzi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores