Nkhani
Timu ya Kukoma Ntopwa Queens yatsimiliza masewero awo mu mpikisano wa COSAFA CAF Women's Championship opanda chipambano pomwe yagonja 5-3 mu masewero awo otsiriza ndi timu ya ZESCO Ndola Girls yaku Zambia masana a lachiwiri.
Timuyi inagoletsetsa zigoli zisanuzi mu mphindi 70 za masewerowa koma Inasewera mosinthika mu mphindi khumi za kumapeto pomwe Rose Alufandika, Kondawo Banda ndi Jessie Yosefe anagoletsa zigoli za Ntopwa kuti achepetseko danga la zigoli.
Timuyi tsopano yatsiriza mpikisanowu opanda point iliyonse kamba koti inagonja ndi Mamelodi Sundowns yaku South Africa Women komanso Beauties FC yaku Namibia 3-0 mmasewero aliwonse.
Iwo achinyitsa zigoli 11 ndi kugoletsa zitatu zokha ndipo tsopano akhale akubwerera m'dziko muno.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores