KARONGA YANDAULA NDI OYIMBIRA
Timu ya Karonga United yadandaula ndi mmene oyimbira anachitira pa masewero awo ndi timu ya Chitipa United pa bwalo la Rumphi ponena kuti penate yomwe anayipatsa Chitipa inali yabodza.
Bernard Mwahimba yemwe ndi team manager wa Karonga ndi yemwe wayankhula mawuwa pomwe wati ngakhale kuti akakumana ndi Chitipa United amakhala masewero abwino, koma oyimbira sanawathandize mmasewerowa.
"Anali masewero abwino komanso ovuta poti tikakumana ndi Chitipa timalimbana kwambiri poti tonse timachokera kumodzi nde tinayesetsa kuti tichite bwino, tinagoletsa nthawi yabwino koma oyimbira sanatithandize mmasewerowa." Anatero Mwahimba.
Iye anati timu yakebe inakanika kuti isewere bwino pa masewerowa kutengera ndi mmene amasewerera koma akabwerera ku Karonga akakonza mavuto awo onse.
Timuyi tsopano yafika pa nambala yachisanu ndi chitatu (8) pomwe ili ndi mapointsi okwana 30 pa masewero 22 omwe yasewera mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores