PHODO ANACHINYA ZIWIRI NDI CRECK
Bungwe la Super League of Malawi lalengeza kuti chigoli chachitatu cha timu ya FCB Nyasa Big Bullets pa masewero awo ndi Creck Sporting Club anagoletsa ndi Maxwell Gasten Phodo osati Ernest Petro ngati momwe oyimbira ananenera koyamba.
Izi zadziwika atatha kuunikiranso chigolichi kuti Petro sanaugunde mpira womwe Phodo anamenya mpaka kukalowa mu ukonde koma poti anauthamangira, zinaonetsa ngati wagunda ndi iyeyo.
Zateremu ndekuti Phodo anagoletsa zigoli ziwiri ndi kuthandizira chigoli cha Babatunde Adepoju komabe mphoto ya osewera bwino pa masewerowa ikadali ndi Gomegzani Chirwa.
Phodo tsopano wagoletsa zigoli zitatu pa masewero awiri omwe Bullets inamenya Chitipa United 4-2 komanso Creck Sporting Club 3-2.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr 📷: MMH photography
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores