"PANO TSOPANO AKUSEWERA NDI WANDERERS" - MWASE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Meke Mwase, wati timu yake ilibe mantha ndi kuchita bwino kwa Bangwe All Stars yomwe posachedwapa yakwanitsa kumenya FCB Nyasa Big Bullets komanso Baka City pomwe wati ikusewera masewero enanso ndi Wanderers.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo achibwereza amu Airtel Top 8 loweruka pa bwalo la Mpira ndipo wati timu yake yakonzeka kuti ikakwanitse kuchita bwino.
"Takonzekera bwino masewerowa amenewa ndipo anyamata akutipatsa chilimbikitso kuti tichita bwino ndithu. Awa ndi masewero ena ndipo Bangwe ikumana ndi Wanderers yomwe ikufunitsitsanso kupambana nde takonzeka." Anatero Mwase.
Iye wati osewera onse alibwino kupatula Mphatso Kamanga yemwe ndi ovulala komanso kuti akhala opanda wachiwiri wake, Bob Mpinganjira, yemwe ali ndi Malawi U-20 ku Mozambique.
Wanderers ikupita mmasewerowa ikutsogola kale 1-0 poti masewero oyamba anapambana pa bwalo la Kamuzu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores