KAUNDA WAPEMPHA MASAPOTA A KARONGA KUKASAPOTA KU RUMPHI
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Oscar Kaunda, wapempha masapota atimu yawo kuti apite akasapotere timuyi ku bwalo la Rumphi komwe akugwiritsa ntchito ngati pakhomo pomwe akukumana ndi timu ya Chitipa United loweruka likudzali.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa ndipo wati ochemererawa amawapatsa mphamvu ndipo pozindikira kuti ndi nkhondo yapachiweniweni pakati pa matimuwa anthuwa akawapatsenso mphamvu.
Kumbali ya masewerowa, iye wati timuyi yakonzeka kwambiri poti pa ndandanda wa matimu sali pa bwino.
"Masewero ofunika kwambiri omwe tikuyenera kuti tichite bwino mwa njira ina iliyonse chifukwa padakali panopa tikuyenera kuti tizitolera mapointsi mmasewero kuti mwina tithereko pabwino nde anyamata akuoneka bwino aliyense alinso bwino." Anatero Kaunda.
Timuyi ili pa nambala yachikhumi (10) pomwe ili ndi mapointsi okwana 29 pa masewero 21 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores