"OSEWERA ANAYIWALA ZAKUGONJA NDI EAGLES" - MUNTHALI
Wachiwiri kwa wothandizira kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wati aphunzitsi atimuyi anawayankhula mowalimbikitsa anyamata awo ndipo padakali panopa akuoneka kuti anayiwala kale.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Civil Service United mu chikho cha Airtel Top 8 loweruka pa bwalo la Kamuzu ndipo wati iwo akonzeka kuti achite bwino.
"Zoonadi tikuchoka kogonja ndi Blue Eagles mu Airtel Top 8 zomwe mu mpira zimachitika, tinawayankhula osewera ndipo anayiwala kale. Tikusewera ndi Civil omwe sakhala masewero ophweka nde sitikuyenera kuyitenga mophweka koma tichilimike." Anatero Munthali.
Iye wati kubwereranso kwa Ernest Petro kukhonza kuthandizira timuyi pakati pawo ndipo akuyembekezera kuti asewera mmene amachitira nthawi zonse.
Bullets ikuyembekezeka kusewera ndi Civil mmasewero achibwereza ku Lilongwe mwezi wa mawa ndipo odutsa adzafika mu ndime ya matimu anayi a mpikisanowu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores