FAM YALANGANSO WANDERERS
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yauzidwa kuti ipereke ndalama yokwana K1.5 million kamba ka ziwawa zomwe ochemerera awo anachita pa masewero omwe timuyi inagonja 2-1 ndi FCB Nyasa Big Bullets mu FDH Bank mwezi wapitawo.
Malingana ndi kalata yomwe yasainidwa ndi mlembi wa bungweli, Alfred Gunda, yati Wanderers yapatsidwa chilango choti ipereke K3 million koma K1.5 million aperekeretu asanasewere masewero awo otsatira.
K1.5 million yaimitsidwa kale kwa miyezi isanu ndi umodzi kuti isapalamulenso mlandu ngati woterewu kamba koti anakwanitsa kuletsa ochemererawa kugendaku.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores