"CIVIL INATIPANIKIZADI LERO" - MWASE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Meck Mwase wati timu yake inakumana ndi masewero ovuta kwambiri pomwe Civil Service United inawapanikiza kwambiri koma wathokoza anyamata ake poteteza mpaka kupambana.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 1-0 pa bwalo la Civo masana a lachisanu ndipo wati timu yake ikufunitsitsa kuti izitolera mapointsi onse atatu kuti izipita kumtunda kwa ligi.
"Lerodi kunatenthadi anyamata a Civil anatipanikizadi munaona anabwera koyamba kuja koma tinakwanitsa kuwakhazika chete nde anali masewero ovuta koma chokoma ndi chakuti anyamata anayikapo mpaka tapambana." Anatero Mwase.
Iye wati timu yake sikuyang'ananso za timu ina pomwe iwo akufunitsitsa kuti azichita bwino ndi cholinga choti aziyandikira kumtunda komwe kuli timu ya Silver Strikers.
Manoma tsopano ali pa nambala yachiwiri mu ligi ndi mapointsi 35 pa masewero 18 omwe asewera mu ligi ndipo akuchepekedwa ndi mapointsi asanu kuti apeze Silver.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores