MADINGA SASEWERA NDI CIVIL
Katswiri wosewera pakati kutimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Francisco Madinga, sapezeka nawo pa masewero omwe timuyi ikumane ndi timu ya Civil Service United masana a lachisanu.
Izi zili chomwechi kamba koti katswiriyu anapatsidwa kalata yofiyira pa masewero omwe timuyi inalepherana 0-0 Premier Bet Dedza Dynamos lamulungu lapitali.
Enanso mwa osewera omwe sapezeka ku matimu awo kamba kosowa mwambo ndi Chifuniro Mpinganjira ndi Khumbo Banda a Premier Bet Dedza Dynamos, Innocent Botomani wa Moyale Barracks, Stain Malata wa MAFCO ndi Chimwemwe Chunga wa Mzuzu City Hammers omwe ali ndi makadi achikasu atatu koma Gabinho Daudi wa Bangwe All Stars analandira kalata yofiyira.
📷: MH Photography ✍️: Hastings Kasonga
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores