"ANYAMATA APUMA TSOPANO" - YASIN
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Rodgers Yasin, wati tsopano osewera atimu yake atha kuchita bwino pa bwalo la Mzuzu chifukwa choti apuma kusiyana ndi zovuta zomwe anaziona akusewera ndi Chitipa United sabata yatha.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Mzuzu City Hammers ndipo wati timuyi ikufunitsitsa kuchita bwino ndi cholinga chofuna kuchoka kumunsi kumene iwowo akhazikika.
"Timakumana ndi zambiri pomwe timapita ku Karonga, galimoto yathu kuonongeka zomwe zinachititsa kuti osewera akhale otopa kwambiri koma apa tsopano apuma, tikapewa zolakwika zomwe tinachita ndi Chitipa ndipo ndikuyembekezera kuti tichita bwino." Anatero Yasin.
Timu ya Bangwe ili pa nambala 15 mu ligi pomwe ili ndi mapointsi Khumi ndi awiri (12) pa masewero 17 omwe iyo yasewera mu ligi ya TNM.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores