SILVER YAPEZA CHIBWENZI CHINA
Timu ya Silver Strikers yapeza bwenzi lina lotchedwa My Gold omwe akhale akuthandiza timuyi pa jersey imene amagwiritsa ntchito.
Izi zadziwika lachitatu pomwe mbali ziwirizi zimasainirana mgwirizanowu wa ndalama yokwana K3 million yomwe kampaniyi izipereka ku timuyi.
Timuyi tsopano izivala jersey tikhala ndi chizindikiro cha My Gold mmbali mwa mikono ya zovalazi pomwe wothandiza wamkulu pa zovalazi ndi Kampani ya Betway.
Kupatula Kampani ya Betway komanso My Gold, timuyi ilinso pa mgwirizano wa thandizo ndi ma Kampani a Mika Greenland, Maybe Tomorrow Fitness and Ziva Security Services.
Chithunzi: Silver media
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores