"TIKUYEMBEKEZA KUCHITA BWINO NDI KB" - KAUNDA.
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Oscar Kaunda, wati timu yake yakonzeka kuti ichite bwino pomwe ikukumana ndi Kamuzu Barracks cholinga asunthe kwambiri pa ndandanda wa matimu mu ligi.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe aseweredwe pa bwalo la Rumphi lachitatu masana ndipo wati timu yake ikufunitsitsa kupeza chipambano choyamba mu chigawo chachiwiri cha ligi.
"Tithokoze Mulungu kuti tayenda bwino kuchoka ku Lilongwe kufika ku Rumphi ndipo tithokoze Mulungu kuti zokonzekera zathu zayenda bwino tamaliza zonse ndipo ndikuyembekezera kuti tichita bwino pa masewerowa." Anatero Kaunda.
Timuyi inagonja pakhomo 1-0 ndi Silver Strikers mmasewero awo oyamba a ligi mchigawo chachiwiri ndipo sabata yatha agonjanso ndi Blue Eagles 2-0 mu chikho cha FDH Bank.
Timuyi ili pa nambala 12 mu ligi ndi mapointsi okwana 19 pa masewero 16 omwe asewera mu ligi ya chaka chino.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores