Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yayamikira timu ya FCB Nyasa Big Bullets kamba kokwanitsa kugonjetsa timu ya Red Arrows yaku Zambia mu mpikisano wa CAF champions league 2-1 lamulungu.
Iwo ati timuyi yaonetsa chamuna ndipo ikachite chomwechi ikapita ku Zambia loweruka kuti apitire mu mpikisanowu.
Iwo wati kuchita bwino kwa timuyi mu Africa muno ndi chimwemwe cha dziko la Malawi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores