Masapota a Dedza Dynamos akusemphana!
Pali chimkulirano komanso kusamvana maganizo pakati pa masapota atimu ya Dedza Dynamos pomwe ena asakugwirizana ndi kuti Andrew Bunya atsogolere timuyi mu 2024.
Mphunzitsiyu yemwe walowa mmalo mwa Gilbert Chirwa ndipo kwawo ndi ku Dedza komweko wayang'anilidwa mmaso ndi ena mwa masapota omwe akuti iye ayitulutsitsa mu ligi ya TNM.
Koma gulu lina la masapotawa ali okwiya ndi zoyankhula za enawa pomwe akuti Bunya ndi mphunzitsi wabwino ndipo akungomukana poti akumudziwa.
Mphunzitsiyu anaphunzitsapo Extreme FC kumapetopeto Kwa masewero awo mu 2023.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores