CHIKHO CHA NYASA CAPITAL FINANCE CHAKWERA NDI K5 MILLION
Kampani yobwereketsa ndalama ya Nyasa Capital Finance Limited yalengeza kuti ndalama zomwe zimapita ku chikho cha mpira wamiyendo cha kampaniyi chakwera kufika pa K70 million kuchoka pa K65 million.
Wapampando wakale wa kampaniyi, Fleetwood Haiya, walengeza izi pa mwambo wokhazikitsa mpikisanowu ku Lilongwe loweruka madzulo. Iye wati akuyembekeza kuti mpikisanowu uthandiza kuonetsa poyera maluso obisika mzigawo zonse.
Ndipo wapampando watsopano wa kampaniyi, Joseph Mononga, wati kampani yawo ipitilira kuthandiza chikhochi kwa zaka zopyolera zitatu zomwe akhalapo kale.
Mu chaka choyamba, chikho cha Nyasa Capital chinali pa K15 million , kenako K25 million chaka chachiwiri chisanafike pa K65 million chaka chatha.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores