Bungwe loyang'anira atolankhani olemba nkhani zamasewero la Swam ladzudzula mlembi wa (Sulom) Williams Banda kaamba kotukwana mtolankhani wa Radio Islam Yusufu Daisa pamene amafuna kuwafunsa mafunso.
Chikalata chomwe bungwe la Swam latulutsa chosainidwa ndi Wesysylas Chirwa chati ndizokhumudwitsa kuti atolankhani olemba nkhani zamasewero akupitilira kukumana ndi nkhanza pamene akugwira ntchito.
Zina zomwe a Banda anayankha wolemba nkhaniyo pa funso lake ndi izi "Clarification yachani? Sizopusazo zimenezo, fixture inatuluka liti? Ndiwe opusaso eti. Osazandiimbiraso,".
A Chirwa kudzera m'chikalatacho ati wolemba nkhani zamasewero akukumana ndi zotsamwitsa zochuluka akamagwira ntchito yawo mabwalo osiyanasiyana mdziko muno.
Padakali pano, Swam yati ineneza zamavutowa ku bungwe la FAM komanso Malawi National Council of Sports.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores